Mtsogoleri wa Dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera adzudzula achifwamba omwe agwetsa network yomwe imagwira ntchito potulutsa ma bukhu opitira kunja (Passports).

Poyankhula munyumba ya Malamulo lero , a Chakwera adachenjeza achifwambawo kuti boma silipereka ndalama zomwe iwo akufuna.

A Chakwera adati kugwetsa network ndi kulakwira malamulo adziko lino komanso ndi kuika dziko pa chiopsezo .

Pachifukwachi, a Chakwera apempha okhudzidwa kuti athane ndi izi masadapite ma sabata atatu. A Chakwera ati iwo monga mkulu wa za chitetezo salora izi kuti zipitilire.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *