Mtsongoleri wa dziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera wati ndi okhudzidwa ndinso a Chisoni ndi imfa ya yemwe adali mtsogoleri wa dziko la Namibia a Dr Gage Gottfried Geingob.

A Geingob adamwalira pa 4 February, 2024 patangotha mwezi umodzi atalengeza kuti iwo apezeka ndi matenda a Khansa.

Chakwera kupereka ulemu otsiliza

A Chakwera ali mu dziko la Namibia pomwe iwo ndi nthumwi zina zili mdzikolo kukhuza maliro a olemekezeka a Geingob.

A Chakwera ati imfa ya Geingob yankhuza Africa komanso dziko lonse lapansi kamba kakuti a Geingob adali munthu olimbikira pa nkhani zolimbikitsa mtendere.

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *