Mkhalakale pa ndale a Ken Msonda adzudzula chipani cha Democratic Progressive (DPP) kamba ka mkhalidwe wake oloza zala kwa anthu wena pamene mavuto akuchoka kwawo komweko. Ken Msonda : DPP ikulakwitsa Mukulankhula kwawo a Msonda apereka chitsanzo cha ziwawa zomwe zidachitika pa Mbowe. Iwo ati palibe amene angapite kukamenya otsatira a chipani cha DPP pakadali pano kupatula okha okha. “Ku DPP kuli magulu magulu omwe akulimbirana ma udindo. Nkhondo ikuchokera komweko, ” adatero a Msonda. Iwo adati mbiri yaziwawa yagona ku DPP. “Kodi adapha Chasowa ndi ndani, nanga Issa Njaunju adapha ndindani?”adafunsa a Msonda. A Msonda adapitiliza kufunsa kuti kodi amene amaotcha misika ndinso kuotcha ma nyumba awanthu ndindani , ndimayesa ndi DPP. “DPP ndi chipani chomwe chikulephera kukonza zinthu zake akatero amafuna kupaka anthu wena,” adatero a Msonda. Post navigation Chakwera mourns Namibian President the late Dr Gage Gottfried Geingob Political and religious intolerance worries catholic Bishops in Malawi