Kafukufuku wa gawo loyamba la kawuniwuni wa m’mene dziko lino lingachitire pa zokolola za kumunda, likuonetsa kuti dziko lino likhoza kukolola chimanga chokwana matani 3.6 miliyoni.

Dr Lazarus McCarthy Chakwera with Sam Kawale

Mlingowu ndi okwera ndi 2.8 percent poyerekeza ndi chaka chatha pamene dziko lino lidakolola matani okwana 3.5 miliyoni.

Nduna ya za ulimi a Sam Kawale yatsimikiza za kawuniwuniyu ponena kuti lipoti lotsiriza lituluka mwezi wa mawa.

Ndipo kawuniwuniyu akuonetsa kuti dziko lino likhoza kukolola mpunga wokwana matani 166,364 umene ndi okwera ndi 38 percent poyerekeza ndi kawuniwuni womaliza wa chaka chatha.

Kawuniwuniyu akusonyeza kuti mlingo wa zokolola zambiri ukhoza kukwera poyerekeza ndi chaka chatha komabe lipoti lomaliza la mmene dziko lino lingachitire ndi limene lifotokoze zonse.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *