Tate wa fuko la Malawi Dr Lazarus McCarthy Chakwera lero kummawaku wayendera msika wa ukulu wa Mzuzu komanso msika wina uja amati wa Vigwagwa. Mukulankhula kwawo a Chakwera anathokoza anthu ochita malonda aku Mzuzu kamba kosunga mwambo nthawi zonse. President Dr Lazarus McCarthy Chakwera Mtsogoleriyu anati boma lake kudzera ku bungwe lija lobwereketsa ndalama la NEEF liwathandiza mavendawa. Chakwera, wati awonetsetsa kuti anthu amene akuchita malonda m’misika ya mdziko lino akupindula kudzera mu ndondomeko yobweleketsa ndalama ya NEEF. Mtsogoleri wa dziko linoyu anati pakali pano boma laika ndalama zoposa K80 billion zoti zithandizire anyamata komanso amayi omwe akuchita malonda ngati mbali imodzi yoonetsetsa kuti akhale odzidalira pa chuma. Mukulankhula kwawo, phungu wa nyumba ya malamulo wa delaro, a Donex Mwamlima anayamikila a Chakwera kamba ka masomphenya ake pankhani za chitukuko m’dziko muno. Iwo apempha a Malawi kuti athandize a Chakwera kukwanilitsa masomphenya amenewa. Post navigation Minister Sam Kawale launches anti Tobacco smuggling campaign Chakwera encourages Mzuzu business owners to benefit from NEEF
As the businessmen are blessed by our president don’t forget needy students under Codel program at Mzuzu university who are struggling for fees. Am one of them 0881652954. Reply