Kudali chimwemwe ndinso chisangalaro m’boma la Karonga pamene mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera adakachereza anthu omwe adakhudzidwa ndi amadzi osefukira mu m’bomalo. Wena sadakhulupilire koma zachitikadi kuona mtsogoleri wadziko kuyenda mtunda wautali wapansi kuchereza anthu omwe adakhudzidwa ndi madzi osefukira amewo. A Chakwera ku Karonga Mukuyankhula kwawo mbomali, a Chakwera analimbikitsitsa anthu mbomalo kuti boma lawo lipereka chisamaliro chokwanila kwa a Malawi okhudzidwawo. Chakwera adapereka katundu osiyana siyana kwa anthu okhudzidwa. Post navigation Air Cargo Mw donates K6million worth of Medical items to Lumbadzi Health Centre Mfumu yaikulu Kyungu iyamikira Chakwera kamba kochereza anthu obvutika ndi madzi osefukira ku Karonga