Mfumu yaikulu Kyungu ya mboma la Karonga yayamikira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kamba kokachereza anthu omwe adataya katundu komanso osiyana siyana kamba kakusefukila kwa madzi mbomalo.

Mvula yomwe idagwa mowirikiza mmaboma a Nkhotakota ndi Karonga idaononga mbewu zochuluka komanso athu ambiri adataya miyoyo yawo.

A Kyungu adati , a Chakwera asonyeza umunthu kamba kosiya chilichonse ndikupeza nthawi yokayendera wanthu.

Chakwera adapereka katundu osiyana siyana kwa anthu omwe adakhudzidwa ndi madziwa.

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *