Tate wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafunira mafuno abwino anthu onse achipembedzo cha chisilamu pomwe dziko lonse lapansi likukondwelera tsiku Eid-Ul-Fitr. Dr Lazarus chakwera wati iyi ndi nyengo yomwe anthu mdziko muno akuyenera kuchita ntchito zachifundo pakati pa anthu posayangana mtundu kapena chipembedzo. Mtsogoleri wa dziko linoyu walimbikitsaso mgwilizano, kulolerana,mnyengoyi kuti chisangalaro cha Eid -ul-Fitr chikhale chapamwamba komaso chatanthauzo. Polankhula kudzera pamakina a internet a Chakwera apempha a Malawi kuti awonetse umodzi, mtima wa chifundo komanso othandiza ena nyengo yomwe anthu achipembedzo cha chisilamu akukondwelera Eld- Dr Lazarus chakwera wati nthawi iyi ndiyofunika kuti ibweretse chimwemwe, mtendere komanso madalitso mnyumba ndi m’mitima ya nzika za dziko lino. Pakadalipano, mneneri wa bungwe la asilamu la MAM Sheikh Dinala Chabulika wapempha asilamu kuti apitilize ntchito zawo zabwino zothandiza chitukuko cha dziko la Malawi. Eid-Ul-Fitr ndi mwambo omwe asilamu amakumbukila kumaliza kusala zakudya komwe kumachitika pamasiku makumi atatu (30). Post navigation MP Msungama donates relief items to Area 23 Moslems Salima Sugar Company geared to make sugar available across the country