Kudali chimwemwe ndi chisangalaro ku Mangochi pamene wapampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Foster Mtandama adalengeza kuti abweretsa mphatso ya ndalama kuchokera kwa mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera. Mukulankhula kwawo iwo adati ndi okomdwa kuti mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera apeleka ndalama zokwana K1.5 Million kuti zithandizire pa chisangalaro cha Eil-Ul-Fitr pa mzikiti wa M’mbaluku boma la Mangochi. A Mtandama popeleka ndalamayi adati ichi ndi chilimbikitso chachikulu chomwe mtsogoleri wa dziko lino ali nacho pa nkhani yazipembedzo mdziko muno. A Mtandama ati asilamu akugwira ntchito yaikulu mdziko muno pa nkhani ya chitukuko komanso malonda mchifukwa chake mtsogoleri wa dziko linoyu anaona kuti ndichinthu chapamwamba kuthandiza mzikitiwu pomwe akusangalala m’nthawiyi. Post navigation Zikhale commends Malawi and Zimbabwe diplomatic relations Be Proud of Your Culture: Irish Ambassador Advises Youth