Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wauza maiko ndi mabungwe kuti dziko anthu 9 Million ali pa chiopsezo cha njala kamba ka ngozi dzodza mwadzidzidzi dzomwe dzinadza kamba ka kusintha kwa nyengo. A Chakwera alankhula idzi pamsonkhano omwe umachitika ku Nairobi Kenya wa atsogoleri a maiko. A Chakwera adati dziko lawo ndi lokonzeka kupanga ubale ndi bungwe ndi dziko lililonse pofuna kupeza mfundo zeni zeni zomwe zikupangitsa kuti dziko lisapindule. Mtsogoleriyu wauza maiko kuti kusowa kwa chakudya ndzomwe zimayambitsa kutsika mphamvu kwa ndalama ya kwacha. Iwo adati boma lake aika ndondomeko zomwe zithandize kubwezeretsa chonde mnthaka komanso kuchotsa mchere. A Chakwera adati, boma lawo lakonza ndondomeko ya zaka makumi awiri yomwe cholinga chakendikubwezeretsa nthaka. A Chakwera ndi m’modzi mwa atsogoleri omwe ali nawo ku msonkhanowu womwe wasonkhanitsa azimtsogoleri amuno mu Africa omwe akhudzidwa kuti awonetsere kufunika kwa feteleza ndi thanzi la nthaka. Msonkhanowu ukuyembekezeka kuvomereza ndondomeko ya zaka 10 yomwe idzapereke malingaliro enieni a zomwe atsogoleri amu Africa ndi ogwira nawo ntchito ayenera kuchita. Mu June m’chaka cha 2006, atsogoleri a mayiko ndi maboma amu African Union (AU) adavomereza chilengezo cha Abuja pa feteleza wa Africa Green Revolution, njira yapadziko lonse lapansi yothetsa vuto lodetsa nkhawa la kusabereka bwino kwa dothi la ku Africa. Post navigation Chakwera spells out 10 year plan to restore soil health Chakwera vows to secure food security in Malawi