Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera lero watsekulira chionetsero chazamalonda mum’zinda wa Blantyre.

Mukulankhula kwawo a Chakwera, adayamikira bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) kamba kokonza mwambo umenewu.

A Chakwera adalimbikitsa a Malawi kuti azipanga nawo katundu ndikumatumiza kunja.

Iwo adati dziko litha kupindula kwambiri ngati likutumiza Katundu wambiri kunja. Iwo adati ndi odabwa kuti a Malawi ambiri amakangalika kugula zinthu zakunja zoti zambiri ku Malawi kuno ziliko.

Koma mukulankhula kwawo mkulu wa bungwe la MCCCI a Dr Wisely Phiri, adayamika boma pamodzi ndi a Chakwera kamba ntchito zomwe bomalo likupanga zomwe adati zithandiza kutukula malonda mdziko muno

A Phiri adapereka chitsanzo cha ntchito za Agricultural Commercialization Project (AGCOM).

Nawo a Sosten Gwengwe omwe ndi nduna ya zamalonda anayankhula mwamphamvu pomwe amauza mtsogoleri wadziko lino kuti panopa nkhani yodalira dzinthu za kunja yayamba kuchepa.

A Gwengwe adapereka chitsanzo kuti Malawi pano idasiya kuitanitsa Tomato kunja komanso nkhuku.

Iwo adati posachedwapa dziko la Malawi lisiya kuitanitsa Cement chifukwa Malawi idzipanga yokha.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *