Tate wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera watsimikizira alimi mdziko muno kuti nthawi yakwana kuti alimi azipindula ndi ntchito yawo.

Chakwera amayankhula izi lero kunyumba yaboma ya Kamuzu Palace ku Lilongwe pamene iye amakumana ndi alimi.

Mukulankhula kwawo a Chakwera adati nthawi yakwana kuti alimi azitumiza ana awo ku ma sukulu abwino.

Iwo adadzudzula mchitidwe opondereza alimi monga kuwagula mbewu zawo pa mtengo otsika.

Iwo adati nkhani ya bwino ndi yakuti ku Malawi kuno zinthu zayamba kuyenda bwino ndipo adati zinthu zikutheka.

“Ndikayang’ana mmene ulimi wa ma Macademia Nuts ukuyendera, kuti pano Malawi iri pa Number 3 mu Africa
yonse, ndikuona kuti zikutheka,” Adatero a Chakwera.

A Chakwera adati akayang’ana m’mene ulimi wa mbatatesi ukuyendera, kuti pano Malawi iri pa Number 1 mu Africa yonse komanso number 2 mdziko lonse lapansi, ndiye kuti zikutheka.

“Ndikayang’ana mmene ulimi wa ma Mega Farm ukuyendera, kuti ma bungwe a boma, komanso ma cooperative ambiri akuyambitsa ma Mega Farm awo, ndikuona kuti zikutheka,” adatero a Chakwera.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *