Nduna yoona za Madzi ndi Ukhondo, Mayi Abida Sidik Mia, omwenso ndi phungu woimila dela la Chikwawa Nkombedzi ku nyumba ya malamulo, wati apitiliza kusintha nkhope ya dela lakeli, pomwaza zitukuko, kuti zifikire anthu onse.

Ndunayi imayankhula izi, pa mwambo woyambitsa ntchito yomanga malo a zipangizo za makono za makina a computa ndi intaneti, pa sukulu ya sekondale ya ku dela ya Nkumanidza Community Day Secondary School (CDSS).

M’mau awo, a Mia anati, kusiyana ndi zaka zinayi zapitazo, pomwe anthu adawavotera asakuwadziwa kwenikweni za kuthekera kwawo pa ntchito za chitukuko, panopa, iwo ndiwokondwa, kuti tsopano anthu awadziwa kudzera mu ntchito za manja awo, maka mu changu chawo, pomwaza zitukuko zapamwamba, ndipo kuti ichi chakhala chikoka chapadera chomwe anthu amawakondera monga njuchi zikondera duwa.

“Anthu anga mwandidziwa tsopano, ndipo ntchito za manja anga zomwe zikundichitira umboni zipitilira kutero kuti chitukuko m’magawo onse chifikire ponseponse kwa anthu onse m’dela lino,” anatero a Mia.

Pa nkhani ya chitukuko chapamwamba chomwe chimakhadzikitsidwa pa Nkumanidza CDSS, a Mia anati ndi okondwa kuti dela lawo lipindula nawo pa ntchitoyi, kamba koti anyamata ndi atsungwana akhala ndi upangiri wa luso la makonoli akadali achichepere, ndipo kuti izi zithandidza kwambiri chifukwa choti tsogolo la dziko lino pa chitukuko lagona mu luso la ma computa ndi intaneti.

M’derali la Nkumanidza lomwe liri ku malire a dziko lino ndi la Mozambique, iwo ngati ngati phungu, a Mia amangako ofesi ya apolisi yamakono pa chipata cholowera ndi kuturuka komanso ali mkati momanga sukulu ya pulaimale yatsopano. Mapulojekiti awiri onsewa akuchokera mu thumba lawo la chitukuko la Constituency Development Fund (CDF).

Malinga ndi mkulu wa bungwe la Macra, a Daud Suleman, ntchito yomanga malo a luso lamakonoli pa Nkumanidza CDSS, ithandidza kuchepetsa vuto la kusowa kwa makina a computer ndi intaneti, kamba koti kumakhala kovuta kuti anthu okhala kumadera akumidzi, athe kupeza computer kapena foni yabwino yomwe angagwiritsire ntchito intaneti.

Ntchitoyi yomwe aigwire ndi ndalama zotsachepera K240 Million idzabweretsa makina a computa 40 ndipo kuti intaneti yaulere (WiFi) idzidzapezeka kwa aliyense pa mamita okwana 100 kudzungulira malowa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *