Mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus Chakwera wati ndi odandaula ndi imfa ya yemwe adali nduna yakale yaboma yoona  za malamulo a Raphael Kasambara.

A Kasambara adamwalira dzana pa 7 June , 2024, mchipinda momwe iwo amagona ku Damron Lodge ku Lilongwe.
Koma mukulankhula kwawo, a Chakwera adati, iwo pamodzi ndi mai wafuko a Monica Chakwera ndi okhudzidwa kwambiti kamba koti a Kasambara adali munthu olimbikira kwambiri kutumikira dziko lino pankhani za Malamulo.
A Chakwera ati, a Kasambara adali munthu odzipereka kwambiri panthawi yomwe iwo amagwira ntchito ku boma ngati nduna yoona nkhani za Malamulo.
Mwa ichi a Chakwera ati a Malawi adzawasowa a Kasambara maka luso lawo pa ukadaulo wa malamulo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *