Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera walengeza kuti sapita nawo ku mwambo olumbiritsa mtsogoleri wa ku South African ameneso ndi bwenzi lake kwambiri, Crill Ramaphosa omwe angowasankha kumene. Mukulankhula kwawo, nduna yoona zofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu ndi amene alengeza izi pamsonkhano omwe unachitika m’muzinda wa Lilongwe. A Kunkuyu adati, m’malo mwake atumiza nduna yoona nkhani zakunja a Nancy Tembo. A Kunkuyu awuzaso msonkhano zosenzi zachitika kuti a President apereke nthawi yambiri ku zichita zokhudza ngozi yomwe yachitika yomwe yakhudza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Dr Saulos klaus Chilima ndi wena asanu ndi atatu (8). Post navigation HRCC hails peaceful co-existence as the country is mourning VP Chilima President Chakwera’s Leadership Shines in Times of Grief