Abida Mia ayambitsa ntchito yomanga chipatala Wolemba: Mtolankhani Wathu Vuto la odwala kuyenda mtunda wautali kukalandira thandizo la chipatala, likhala mbiri yakale kwa anthu okhala modzungulira dela la Masukambiya kwa Mfumu yaikulu Ngabu m’boma la Chikwawa, potsatira ntchito yomanga chipatala yomwe nduna yowona za Madzi ndi Ukhondo, Abida Mia, omwenso ndi phungu wa dera la Chikwawa Nkombedzi yakhadzikitsa. Mkuyankhula kwawo pambuyo poika mwala wamadziko pa malo pomwe pagwiridwe ntchitoyi, a Mia anati ndi okondwa kuti khumbo lawo loti anthu mderali akhale a moyo wathanzi tsopano likukwaniritsidwa. Chipatala cha tsopanochi chomwe achimange ndi thandizo la ndalama pafupifupi K146 Million kuchokera ku banki yaikulu pa dziko lonse ya World Bank achimanga kwa miyezi itatu. Chikadzatha, chipatalachi chidzathetsa mavuto oyenda mtunda wautali woposa makilomita 13 kukafika ku chipatala cha boma ku Nchalo zomwe zimapangitsa kuti ntchito za umoyo zidzibwelera m’mbuyo. Powonjedzera pa ntchitoyi, ngati phungu wa derali, a Mia agwiritsa ntchito ndalama za mthumba la chitukuko cha ku dera, la CDF pomanga nyumba ziwiri zogona ogwira ntchito pa chipatalapo. Anthu oposa 15,000 ochokera m’midzi yodzungulira Nyakwawa Masukambiya ndi omwe adzidzalandira thandizo pa chipatalachi. Aka sikoyamba a Mia kuwonetsa chidwi pa ntchito zotukula umoyo wa anthu mderali kamba koti chikhalireni phungu akwaniritsa kumanga chipatala cha Therere komanso zipatala zoyeza pa sikelo ana osapyola zaka 5 ku dela la Mchenga ndi Saopa. Mayi Mia adachitanso chotheka kugwiritsa ntchito thumba la CDF kumanga nyumba yachisoni pa chipatala cha Ngabu komanso kupereka ma ambulansi awiri ku chipatala cha Therere ndi ina yotumikira mdela lonse la Mkombedzi. Mchaka cha 2019 pamene ankapanga misonkhano yokopa anthu, a Mia adalonjedza kuti adzaonetsetsa kuti athu sakuyenda mtunda woposa khumi kuti apeze chipatala. Post navigation CHRR challenges media to advance tackling Sexual and Reproductive Health related Issues Chakwera saves Southern Region from hunger via cash transfer program