M’mbiri ya zoimba imba mdziko muno, Paul Chaphuka ndi m’modzi mwa oimba yemwe amapatsidwa ulemu kwambiri kamba ka luso lake.
Chaphuka adatulutsa chimbale chimodzi basi cha Ndichilitseni koma adatchuka kuposa oimba wena omwe ali ndi zimbale zankhani nkhani.
Chaphuka adamwalira pa 11 May, 1997 koma adamaliza chimbale chimenechi adali azibale ake a Paul ndi Lucius Banda.
Chaphuka adafa ndi matenda a cancer ya pakhungu.
Luso la Chaphuka lidaoneka pomwe iye amaimba ndi Mteweti Wambali Mkandawire. Munthu uyu adali odabwitsa kwambiri. Kawiri kawiri aluso oimba zida sakwanitsa kuimbaso mau.
Koma Chaphuka amaimba chida chilichose pa band kuphatikizaponso mawu. Adali ndi mau apamwamba kwambiri komanso anthetemya.
Ataimba ndi Wambali nthawi yaitali adaganiza kubwerera kumudzi kwawo ku Balaka komwe adakajoina band yotchuka kwambiri ya Alleluya yomwe nthawi imeneyo imatsogoleredwa ndi PaulBanda.
Kumeneku iye adapatsidwa chida cha lead guitar kuti aziimba chimenecho.
Komano anthu wena amene akudziwa bwino za mmene zimayendera , Paul amatha kuthandizira paliponse pomwe pakufooka kuphatikizapo ma keyboards.
Chimbale chimenechi chidali ndi nyimbo zambiri monga;  Nkhoswe, Ndichiritseni, mavuto tawaona.
Akumaliza chimbale Paul ndi Lucius Banda adaikamo nyimbo yotchedwa Tsalani.
Iye adagwira ntchito ndi mizwanya ina mmaimbidwe monga Paul Subiri, Coss Chiwalo, Pati Abig Tung’ande, Malemu Lucius Banda Rodrick Valamanda, Charles Sinetre ndi wena otere.
Tizawakumbukira bwanji a Paul Chaphuka? Pakufunika chaka ndi chaka pazikhala show ku Balaka kukumbukira Legend ameneyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *