Mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati ophunzira akuyenera kuonetsa luso lawo pa zomwe aphunzila pochita ntchito zosiyana-siyana m’dziko muno. Chakwera wayakhula izi pomwe ophunzila oposa 2000 pa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu amalandila mapepala awo osanyeza kumaliza maphunzilo. A Chakwera ati ophunzirawa akuyenela kuonetsa lusoli m’magawo a zachipatala, zandale, kayendetsedwe kabwino ka boma, zaluso mwa zina. “Sichikhala chopindula kungokhala ndi nzelu za m’mabuku koma aliyense wa inu akuyenela kuchilimika kuti dziko lino likwanitse masophenya ake a Malawi 2063 pomwe tikufuna kutukuka mu magawo a zokopa alendo, zaulimu komanso ntchito za migodi,” a Chakwera anatelo. Mtsogoleli-yu anawonjezelanso kuti ntchito yotsegula mphamvu zatsopano zamagetsi ku Choma zithandizanso kuti dziko lipite patsogolo ku khani ya zokopa alendo mwa zina. Ndipo iye anati ndithandizo lochokela ku World bank mu mapulogalamu osiyanasiyana monga African centers of excellence ndi ndalama yosachepela 30 million dollars komanso pologalamu ya Skills for vibrant economy ya ndalama yosachepela 100 million dollars dziko lino likhala ndi ukadaulo okwanila pa ntchito za luso. A Chakwera atinso dziko lino likupita patsogolo mu khani yobwenzeletsanso chikhulupililo kwa maiko a kunja ku mbali ya khani za kubwenzeletsa chilengedwe, malonda a maiko a kunja komanso khani za ufulu wa aliyense ndi ndale zosakondela. Post navigation Chakwera urges graduates to help fix the country’s problems President Chakwera honoured with doctorate degree for his ability to foster bilateral relations