Lipoti la ngozi yomwe idapha wachiwiri kwa mtsogoleli wa dziko lino a Dr Saulos Klaus Chilima ndi athu ena asanu ndi atatu lomwe bungwe la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation (BFU) lidapanga lati, ndege idagwa kamba ka chifunga choipa chomwe chidali kudela la kumpoto nthawi ya ngoziyo. Mwazina lipoti-li likufotokoza kuti ndege-yi inali ndi mafuta okwanira kuuluka kwa maola awiri komanso kupitilira, komanso kuti oyendetsa ndenge-yi anayesa kuulukila nayo ku Ekwendeni pomwe anauzidwa kuti ku Mzuzu sikunali koyenelela. Kuphatikiza apo ndenge-yi inayesa kuuluka pamamba pankhalango ya Chikangawa isanangwe ndipo kuti mu ndenge-yi munalibe chida chotapira mawu (Data Recorder and Cockpit Voice recorder) komanso chida chothandiza kuti adzitha kulumikizana ndi anzawo apafupi chinali chokutha kuchokela m’chaka cha 2004. Ndipo lipoti-li likupitilizanso kunena kuti ndenge-yi inagwa itaomba mtengo wa mulingo wa ma mitala oposela anayi. Ndipo kumapeto lipoti-li lafotokozanso kuti popima matupi a anthu omwe anafa pangozi-yi zinaonetsa kuti anthu-wa anamwalila chifukwa cha khawa zomwe analinazo kaamba ka ngozi-yi. Ndipo akatswiri omwe amachita kafukufuku wa ngozi-yi apeleka ndondomeko zofunikira kutsatidwa kwa nduna yoona za chitetezo, komanso ya zamtengatenga pofuna kuti ndenge zonyamula anthu m’dziko muno zizikhala ndi zoyenelela zonse. Post navigation Chakwera rewards Senior Counsel position to Justices of appeal Chakwera akhuza imfa ya Willie Zingani