Mafumu andodo akunsi kwa mtsinje wa Shire adzudzula mtsogoleri wakale wadziko lino a Peter Mutharika kamba kopita kumalowa popanda mafumu kudziwa. Mafumuwa ati monga mwachizolowezi wandale aliyese akamapita kumalo kumalo amayamba wauza mafumu ndicholinga choti agoneke wanthu mmudzi zomwe akuti sizidachitike ndi a Mutharika. Mafumuwa ati zomwe apanga a Mutharika ndikulakwa kwakukulu ndipo asonyeza kuti sakupereka ulemu kwa mafumu. “Kodi ngati a Mutharika akupanga zodelera mafumu panopa nanga akazatenga boma ife azatiyesa ngati anthu? Apapa ndiwachenjeze aMalawi asatengeke ndi madzi odutsa Chakwera sakuyenera kuchoka pampando,” Posachedwapa katswiri pankhani za ndale komanso yemwe amalankhulapo pankhani zachuma Dr Ben Dzolowere, adadzudzula mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) a Professor Peter Mutharika kuti chomwe akufuna sakuchidziwa. A Dzolowere amayankhapo pankhani zomwe zikumveka kuti Mutharika wayamba kuyenda mmaboma a kum’mwela komwe akumema anthu kuti akalembetse mukaundulo wa mavoti. Iwo adati posachedwapa chipani cha DPP chakhala chikupangitsa misonkhano ya atolankhano komwe chipanichi chakhala chikunenetsa kuti ntchito ya kalembera wa mavoti sikuyenda bwino. “Chipani cha a Mutharika cha DPP chakhala chili kaliki kuti anthu asapite kokalembetsa koma posachedwapa taona a Mutharika akupita kokalembetsa ndipo pompano taonanso iwo akuyenda ku Chigwa cha Shire komwe akumema anthu kuti akalembetse izi zikuonetsa kuti a Mutharika palibe chomwe akufuna koma kungofuna kuthana ndi mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera,” adatero iwo. Post navigation Minister Ng’oma commits to support improve service delivery agenda at immigration MCP is the only party in Lilongwe