Boma la Malawi lalandila ndalama zokwana 16Million Euros zomwe ndi pafupifupi K30Billion ndalama za ku Malawi. Mukuyankhula kwawo pa mwambowu, nduna ya za chuma a Simplex Chithyola Banda apempha aliyese okhudzidwa kuti agwiritse ntchito ndalama zomwe zafikazo mwandondomeko yake. Minister of Finance Simplex Chithyola Banda A Chithyola adachenjeza aliyese kuti asayesere dala kuononga ndalama monga izi. A Chithyola ati mgwirizano womwe wasainidwa lero uthandiza kwambiri kupititsa pagolo umoyo wa achinyamata mdziko muno. Mmawu ake nduna ya za umoyo a Khumbize Chiponda adayamika boma la German kamba thandizo lomwe adati lithandiza kuthetsa mabvuto omwe achinyamata akukumana nawo. Post navigation Chakwera says NPC instrumental in Malawi’s development: Zikhale hints on the welfare of police officers