Mfumu yaikulu Kyungu ya mboma la Karonga yayamikira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kamba kokachereza anthu omwe adataya katundu komanso osiyana siyana kamba kakusefukila kwa madzi mbomalo. Mvula yomwe idagwa mowirikiza mmaboma a Nkhotakota ndi Karonga idaononga mbewu zochuluka komanso athu ambiri adataya miyoyo yawo. A Kyungu adati , a Chakwera asonyeza umunthu kamba kosiya chilichonse ndikupeza nthawi yokayendera wanthu. Chakwera adapereka katundu osiyana siyana kwa anthu omwe adakhudzidwa ndi madziwa. Post navigation Chakwera apereka chikhulupiliro kwa wanthu okhudzidwa ndi madzi osefukira m’boma la Karonga Lilongwe City Mayor Richard Banda hails Japanese Government for the signing of Ambulance grant