Tiwadziwe a Jiya Posachedwapa Phungu wa Lilongwe City Centre adalengeza kuti akaima nawo pa m’mando wa wamkulu wa achinyamata kuchipani cholamula cha Malawi Congress(MCP). Tinachitika mwayi kukacheza nawo a Jiya kuti tikamve kuti iwo ali ndi maso phenya otani. Jiya ndi mmodzi mwa mikhala kale mu chipani cha Malawi Congress. Jiya amadziwika bwino ndi mbiri ya zitukuko mdela lake la Chigawo cha Lilongwe City Centre. Tikunena pano Lilongwe City Centre Constituency silinso chimodzimodzi Jiya akuima pa mpando wa mkulu wa achinyamata muchipani cha Malawi Congress party convention ikubwerelayi. Jiya amene boma la DPP linamumangapo kawiri konse ndi olimba mtima, ofikilika komanso olimbikira. Iye wati ayenela kumvera ndi kuteteza Pulezidenti Chakwera, ma Regional Chair onse, ma DC komanso chipani cha MCP. Iye wati adindo onse osakhidwa kaya ndima MP kapena ma Khansala azapasidwa ulemu oyenelera. Jiya walonjeza kusintha miyoyo ya achinyamata kuti isinthe komanso walonjeza kuti adzagwira ntchito yoonotsetsa kuti achinyamata mzigawo zonse apeza mwai wa ntchito zakunja komanso mMalawi momuno komanso mwayi wangongole. Post navigation Undule hails Chakwera for the Malawi’s State of Disaster Declaration Due to El Niño Weather Patterns Nyumba ya boma yatsutsa mphekesera zomwe nyuzipepala ina mdziko lino yafalitsa zokhudza malipiro