Kudali chimwemwe ndi chisangalaro ku Mangochi pamene wapampando wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Foster Mtandama adalengeza kuti abweretsa mphatso ya ndalama kuchokera kwa mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera.

Mukulankhula kwawo iwo adati ndi okomdwa kuti mtsogoleri wa dziko lino a  Chakwera apeleka ndalama zokwana K1.5 Million kuti zithandizire pa chisangalaro cha Eil-Ul-Fitr pa mzikiti wa M’mbaluku boma la Mangochi.

A Mtandama popeleka ndalamayi adati ichi ndi chilimbikitso chachikulu chomwe mtsogoleri wa dziko lino ali nacho pa nkhani yazipembedzo mdziko muno.

A Mtandama ati asilamu akugwira ntchito yaikulu mdziko muno pa nkhani ya chitukuko komanso malonda mchifukwa chake mtsogoleri wa dziko linoyu anaona kuti ndichinthu chapamwamba kuthandiza mzikitiwu pomwe akusangalala m’nthawiyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *