Mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera watsindika za kufunika kwa ubale omwe ulipo pakati padziko lino ndi dziko la Iceland.

Polankhula pa mgonero omwe anakonzera nduna yaikulu yadziko la Iceland a Bjarni Benediktsson, adati dziko la Iceland ndi bwenzi leni leni losaona nkhope.

Iwo adayamikira dziko Iceland kuti likafuna kuthandiza limathandiza ndi mtima onse mosabwerera m’mbuyo.

Iwo adati ndi okondwa kwambiri kamba ka kubwera kwa a Benediktsson kudzacheza mdziko muno.

A Chakwera adati ulendo umenewu ndi chitsimikizo cha ubale wabwino omwe ulipo pakati pa dziko la Malawi ndi dziko la Iceland omwe upindulire a Malawi.

Iwo adati ngakhale dziko la Iceland limapereka thandizo kumaiko ambiri mu Africa koma limapereka moonjezera kudziko lino la Malawi.

A Benediktsson adafika dzulo kuno ku Malawi kudzera ku Kamuzu International Airport. Ndipo wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Dr Saulos Klaus Chilima ndi omwe adakamulandira mlendoyu yemwe akhala masiku asanu ali kumdziko muno.

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *