Kunali chimwemwe ndinso chisangalaro ku Kamuzu Palace ku Lilongwe komwe mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera adakonzera nkhomaliro nduna yaikulu ya dziko ya Iceland a Bjarni Benediktsson.

Mukulankhula kwawo a Chakwera adati ndi okondwa kwambiri kamba ka kubwera kwa a Benediktsson kudzacheza mdziko muno.

A Chakwera adati ulendo umenewu ndi chitsimikizo cha ubale wabwino omwe ulipo pakati pa dziko la Malawi ndi dziko la Iceland.

Iwo adati ngakhale dziko la Iceland limapereka thandizo kumaiko ambiri mu Africa koma limapereka moonjezera kudziko lino la Malawi.

A Benediktsson adafika dzulo kuno ku Malawi kudzera ku Kamuzu International Airport. Ndipo wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Dr Saulos Klaus Chilima ndi omwe adakamulandira mlendoyu yemwe akhala masiku asanu ali kumdziko muno.

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *