Kwanthawi yoyamba patapita zaka 13, dziko la Malawi layamba kudyerera zipatso za ubale wabwino omwe ulipo pakati pa dziko la Malawi ndi maiko akunja.

Tikunena pano bungwe lalikulu pankhani zachuma la International Monetary Fund (IMF) komanso maiko a Norway, Germany, USA, UK komanso maiko ambiri amumgwirizano wa maiko aku Europe a European Union (EU) nawo ali kalikiliki kuthandiza Malawi.

Nayo Banki yaikulu ya World Bank sikutsalira mmbuyo. Yapereka kale ndalama za nkhani nkhani kudziko la Malawi.

Pakadali pano dziko la Iceland nalo silikutsalira mbuyo. Dzikoli kudzera kunduna yake yaikulu a Iceland a Bjarni Benediktsson yalonjeza kuthandiza dziko la Malawi pankhani za umoyo, za maphunziro, za madzi ndi ukhondo komanso za ulamuliro wabwino.

Ndunayi ili mudziko muno kuyendera ntchito za chitukuko ndipo dzulo pa 21 May 2024, anali ku ku Mangochi.

 

 

 

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *