Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera lero watsekulira chionetsero chazamalonda mum’zinda wa Blantyre. Mukulankhula kwawo a Chakwera, adayamikira bungwe la Malawi Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) kamba kokonza mwambo umenewu. A Chakwera adalimbikitsa a Malawi kuti azipanga nawo katundu ndikumatumiza kunja. Iwo adati dziko litha kupindula kwambiri ngati likutumiza Katundu wambiri kunja. Iwo adati ndi odabwa kuti a Malawi ambiri amakangalika kugula zinthu zakunja zoti zambiri ku Malawi kuno ziliko. Koma mukulankhula kwawo mkulu wa bungwe la MCCCI a Dr Wisely Phiri, adayamika boma pamodzi ndi a Chakwera kamba ntchito zomwe bomalo likupanga zomwe adati zithandiza kutukula malonda mdziko muno A Phiri adapereka chitsanzo cha ntchito za Agricultural Commercialization Project (AGCOM). Nawo a Sosten Gwengwe omwe ndi nduna ya zamalonda anayankhula mwamphamvu pomwe amauza mtsogoleri wadziko lino kuti panopa nkhani yodalira dzinthu za kunja yayamba kuchepa. A Gwengwe adapereka chitsanzo kuti Malawi pano idasiya kuitanitsa Tomato kunja komanso nkhuku. Iwo adati posachedwapa dziko la Malawi lisiya kuitanitsa Cement chifukwa Malawi idzipanga yokha. Post navigation Iceland Government pledges additional support for Malawi Chakwera for more exports