Mkulu wa bungwe loona za malonda la Confederation of Chambers of Commerce and Industry (MCCCI) a Dr Wisely Phiri ayamikira Mtsogoleri wa dziko lino a Dr Dr Lazarus McCarthy Chakwera pa ndondomeko zomwe iye waika pofuna kuti chuma chibwerere mchimake.

Mukulankhula kwawo pamwambo otsekulira chionetsero cha zamalonda ku Blantyre, a Phiri anati bungwe lawo ndi lokhutira kuti chuma chibwerera mchimake pompano.

A Phiri adapereka chitsanzo cha ntchito zomwe zili ku unduna wa za ulimi kuphatikizapo ntchito ya Agricultural Commercialization Project (AGCOM).

A Dr Phiri anati AGCOM ndi ndi njira yabwino yomwe ipangitse kuti Masomphenya a ulimi, migodi zikwanilitsidwe (ATM) zikwanilitsidwe.

Koma a Phiri anadandaula ndikupempha boma kuti liunike bwino ganizo la boma lodula 40% la phindu la ndalama zomwe ma kampane amapanga.

Iwo adati mfundo iyi itha kugwetsa ulesi makampani kuti asakhazikike mdziko.

 

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *