Nduna yaikulu ya dziko la Iceland a Bjarni Benediktsson abwerera kumudzi kwawo ku Iceland dzulo atamaliza ulendo wawo wa masiku asanu. A Benediktsson adafika mdziko muno pa 19 May, 2024, kudzera pa bwalo za ndege pa Kamuzu International Airport (KIA). Ali mdziko muno , a Benediktsson adakayendera zitukuko zosiyana siyana zomwe dziko lawo likuthandiza ku Mangochi. Komanso a Benediktsson ali mdziko muno adachitanso zokambira zapadela zokhudza ubale wa maiko awiriwa ndi mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera kunyumba ya boma ya Kamuzu Palace. Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino a Saulos Klaus Chilima yemwe adaperekeza mlendo olemekezeka kwambiriyu pa Kamuzu International Airport. Koma asadanyamuke a Benediktsson ndi a Chakwera adapangitsa msonkhano wa atolankhani. Ali kumeneko , a Benediktsson alonjeza kupitiliza kuthandiza dziko la Malawi. Komwekonso, a Chakwera adati ndi okondwa kuti zolinga za ulendowu zakwanilitsidwa. A Chakwera adati anawaitana a Benediktsson kuti akawathokoze okha pantchito yaikulu yomwe Iceland akugwira mdziko muno. Iwo adati anamuitananso Benediktsson ndi cholinga choti azadzionere yekha m’mene ndalama zawo zikugwirira ntchito. Post navigation Chakwera waulura njira zammene Chuma cha dziko lino chingapitire patsogolo Bungwe la MCCCI limtaira kamtengo Chakwera pankhani ya dongosolo la dzachuma