Tate fuko la Malawi Dr Lazarus McCarthy Chakwera wabwera poyera kulangiza a Malawi njira zomwe akuyenera kutsata ndi cholinga cholinga chokweza chuma cha dziko lino. Mukulankhula kwawo ku Blantyre pamwambo otsekulira chionetsero cha chazamalonda , a Chakwera anati nthawi yakwana yoti a Malawi ayambe kupanga katundu wawo. A Chakwera adati, Katundu akapangidwa akuyenera kutumizidwa kunja. Mwamsanga zikatere dziko limakhala ndi ndalama zambiri zakunja (forex). A Chakwera apempha a Malawi kuti tiyeni nthawi yakwana ngati dziko, tiyambe kupanga katundu wambiri komanso wabwino kuti athe kupita kunja. Iwo adati ndi okondwa kuti ulimi wa fodya wayamba kuyenda bwino pano zomwe zathandizanso kulowetsa ndalama zakunja. Pakadali pano kafulu akusonyenya kuti Malawi imaoninga ndalama zokwana $3billion pakugula katundu wakunja pomwe $2billion yokha ndiyomwe timapeza kuchokera kunja. Post navigation Chakwera for more exports Mlendo olemekezeka kwambiri nduna yaikulu ya dziko la Iceland a Bjarni Benediktsson abwerera kumudzi kwawo