Mtsongoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera ndi mai Monica Chakwera wafika kumudzi.

Chakwera adachoka kuno ku Malawi pa ulendo wa ku dziko la Namibia komwe adakakhala nawo pa mwambo oyika m’manda Dr Gage Gottfried Geingob.

Chakwera wafika m’dziko muno kudzera ku bwalo la ndege la Kamuzu International (KIA) ku Lilongwe.

President Dr Lazarus McCarthy Chakwera kuyendera perete wa ulemu

Poyankhula m’mau ake ali ku Namibia Chakwera adati ndi okhudzidwa ndinso wa Chisoni ndi imfa ya yemwe adali mtsogoleri wa dziko la Namibia a Dr Gage Geingob.

A Chakwera ati imfa ya Geingob yankhuza Africa komanso dziko lonse lapansi kamba kakuti a Geingob adali munthu olimbikira pa nkhani zolimbikitsa mtendere.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *