Nkhani yokoma. Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera wati bungwe la University Innovation UniPod Centre lomwe lakhazikitsidwa pa Malawi University of Business and Applied Sciences ku Blantyre, lapereka chitsanzo chabwino cha momwe maphunziro apamwamba akuyenera kukhalira. Dr Chakwera ayankhula izi ku school ya Mubas ku Blantyre komwe amakhazikitsa malo omwe bungwe la UNDP lapereka ndalama zokwana $2 milion zomangira malowa. Dr Lazarus McCarthy Chakwera A Chakwera, ati malowa athandizira kusintha malingaliro atsopano kukhala owona. A Chakwera awonjezera kuti malowa athandiza Amalawi kupanga zinthu paokha pothandiza kuti dziko lino litukuke komanso lidziyimire palokha.Iye anati ichi ndi chitsanzo chatukuko cha makono. “A Malawi anzanga, taonani chitukuko chamakono. Oti ife amene tinapita ku University masiku am’mbuyomu, tikumasilira ndithu. Ngakhale ndinali ku Chanco nthawi imeneyo, ndinkabwera kuno kuzacheza ndi a First Lady akuphunzira pano, ndipo zinkaonekeratu nthawi imeneyo kuti kuno a Ngwazi anamanga sukulu yapamwamba. Ndiye sizingakhale bwino kuti munthawi yathu tizimanga ma structure a substandard, ” adatero a Chakwera.. Post navigation Business Mogul Mpinganjira Builds Cancer Hospital in Honour of late Wife Chakwera storms MRA Inland Examination Centre to get fresh update