Mkhalakale pandale a Ken Chitatanga Msonda atuluka chipani cha DPP ndipo alowa chipani cholamula boma cha Malawi Congress.

Polankhulapo mu mzinda wa Mzuzu a Ken Msonda ati aganiza zolowa chipani cha MCP chifukwa cha utsogoleri wa masomphenya wa Dr Lazarus chakwera komanso kamba ka mfundo zabwino za ufulu pa ndale zomwe chipani cha Malawi Congress chikutsatira polamulira dziko lino.

A Msonda adati ino ndi nthawi yoti chipani cha DPP chiphunzire ndale zenizeni osati zolowera pa windo zomwe zikupangitsa kuti chipani cha DPP chizitengedwa kuti chipani cha mtundu umodzi okha.

Dr Lazarus McCarthy Chakwera

A Msonda adati ngakhale chipani cha DPP chitasokosa motani sichingagwetse Dr Lazarus chakwera ngakhale masankho atakhalako mawa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *