Boma, kudzera ku unduna woona nkhani za chuma udachotsa msonkho pa katundu wa kaunjika m’dziko muno potsatira dandaulo lomwe ma venda ndi ogulitsa kaunjika anakatula kwa mtsogoleri wa dziko lino President Dr Lazarus McCarthy Chakwera masiku apitawa ku Kamuzu Palace ku Lilongwe.

Chakwera kukumana ndi anthu ochita malonda

Bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) lasindika za izi mu chikalata chomwe latulutsa.

Izi zadza pomwe ma venda ndi ogulitsa amachita dziwonetsero ku Lilongwe pokakamiza boma kuti litsitse misonkhoyi popeza yakweza belo la zovala za kaunjika kuchoka pa K250,000 kufika pa K700, 000.

Koma zadziwika kuti President Dr Chakwera analamula unduna wa za chuma kuti uchotse misonkho yatsopanoyi ndipo boma lidachotsa.

Koma kafukufuku wathu akusonyeza kuti Boma lidaimitsa kale kale ndalama za misonkho imeneyi pa ma belo a zovala.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *