Sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Science (MUBAS) yapereka ulemu wapadela kwa mtsogoleri wadziko lino a Dr Lazarus McCarthy Chakwera kukhala Tate wa school imeneyo pamwambo omwe unachitikira pa sukuluyo mumzinda wa Blantyre. Mukulankhula kwawo, pamwambo umenewo, a Chakwera Chakwera analandilidwa ndi akulu akulu osiyana aboma kuphatikizapo wampando wa sukuluyi a George Yobe Kanyama Phiri. Atamaliza mwambo umenewu a Chakwera anakhala mlendo olemekezeka pamwambo opereka ma pepala kwa ana 114 omwe amaliza sukulu yawo pa sukulu imeneyo. Ena mwa maphunziro omwe amaliza ndi monga kuona zomanga manga , zowerengera ndalama, zakayendetsedwe ka malonda, zoona kagulidwe ka katundu. Sukulu ya MUBAS yomwe kale imatchedwa Polytechnic, inatsekulidwa mchaka cha cha 1965 ndipo adaisintha dzina kukhala MUBAS mchaka 2021. Post navigation Chakwera presides over first ever MUBAS graduation Sindidzalema kukusakirani thandizo lotukulira madera anu – Chakwera