Mafumu a mboma la Mzimba lolemba adakumana ndi m’tsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera kunyumba ya boma ku Kamuzu Palace mumzinda wa Lilongwe.

Cholinga cha ulendo umenewo kunali kupepesa maliro a yemwe anali wachiwiri wawo a Saulos Klaus Chilima yemwe adafa mwadzidzidzi pangozi ya ndege mu nkhalango ya Chikangawa ku Mzimba pa 10 June, 2024.
Mukuyankhula kwawo, Inkosi ya Makosi M’mbelwa adati mafumu ali ndi chisoni kamba ka imfa ya a Chilima. Mafumuwo adayamika a Chakwera kamba ka uthenga wawo oyanjanitsa a Malawi.
Mukulankhula kwawo, a Chakwera adati, boma lawo lakhazikitsa kauniuni wapadeka kuti choona pa nkhaniyi chidziwike.
A Chakwera adati a Chilima adali anzawo kwambiri ndipo amakhala nawo bwino.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *