Tate wa Dziko Dr Lazarus Chakwera pamodzi ndi Mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera lero anakakhala nawo pamwambo oika thupi la Katswiri pa nkhani za maimbidwe a Lucius Banda. Naye wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Dr Michael Usi anakakhala nawo pa mwambowo. Mukulankhula kwawo komwe anayankhula kudzera kwa nduna ya za maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, adati boma lawo lidzasamalira banja lomwe wasiya Lucius Banda. Chakwera watsimikizira banja la Lucius Banda kuti Boma lisamalanso katswiri wina oumba yembe mkulu wake wa Lucius Banda awa ndi a Paul Banda omwe akhala akubvutikirapo mthupi. A Chimwendo adati a Lucius Banda adali omenyera ufulu wa anthu osuka choncho imfa yachotsa munthu ofunikira kwambiri yemwe adali kazembe wa anthu osauka. Iwo adati a Lucius Banda asiya ntchito yosamaliza monga lamulo loyimira anthu alunso mdziko muno lomwe silimadutse kunyumba yamalamulo. Popitiliza ndi kukhuza imfa ya a Lucius Banda, a Chimwendo adati Malawi waluza munthu amene anali tsanamira pankhani zamaimbidwe mdziko muno. Post navigation CHRR challenges media to advance tackling Sexual and Reproductive Health related Issues Tidzamulira Lucius Banda mpaka kale kale – watero yemwe adaimilira mtsogoleri wadziko lino a Richard Chimwendo Banda