Nduna ya za maboma ang’ono ndi chitukuko cha kumudzi, a Richard Chimwendo Banda auza khwimbi la anthu lomwe lodasonkhana ku Balaka lero kuti dziko la Malawi lidzawalira a Lucius Banda mpaka kale kale. Mukulankhula kwawo mmalo mwamtsogoleri wa dziko lino a Lazarus McCarthy Chakwera , a Chimwendo adayamikira ntchito zabwino zomwe malemu Lucius Banda adagwira kudziko lino la Malawi. Iwo adati iwo amaimba nyimbo za uthenga wamphamvu monga mmene adaimbira nyimbo ija yoti paulendi. A Chimwendo adati utbenga wa nyimbo imene ija ndi wamphamvu kwambiri ndipo ukhala ukutumikira kwa achinyamata mpaka kale kale. A Chimwendo atsimikizira banja la Lucius Banda kuti Boma la Dr Lazarus Chakwera lisamalanso banja la a Lucius Banda pamodzi ndi achimwene awo a Paul. A Chimwendo adati a Lucius Banda adali omenyera ufulu wa anthu osauka choncho imfa yachotsa munthu ofunikira kwambiri yemwe adali kazembe wa anthu osauka. Iwo adati a Lucius Banda asiya ntchito yosamaliza monga lamulo loyimira anthu alunso mdziko muno lomwe silimadutse kunyumba yamalamulo. A Banda asiya mkazi , ndi ana atatu. Post navigation A Chakwera alonjeza kusamala banja la Malemu Lucius Banda Chakwera describes late Banda as a patriotic citizen