Chakwera akhazikitsa gawo lachitatu lofufuza za ngozi ya ndege

Kondanani Chilimunthaka

Gawo lachitatu komanso lomaliza lofufuza zokhudza ngozi yomwe inachitika mdziko muno munkhalango yachikagawa pa 10 Juni chaka chino lakhazikitsidwa lero lolemba pa Okotobala 28, ku nyumba ya boma ya Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe pomwe Pulezidenti Lazarus Chakwera watsogolera mwambo olumbilitsa makomishonala okwana omwe wawasankha kuti akhale akugwira ntchitoyi mpaka kumapeto a mwezi wa Novembala.

Polankhula italumbilitsidwa komiti ya ma komishonalayi, Mtsogoleri wa dziko lino wati anayika ntchito ya kafukufuku wa ngozi ya ndegeyi yomwe inali ya gulu la nkhondo la Malawi Defence Force (MDF) ndipo patsiku langoziyi inanyamula amene anali Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino, malemu Saulos Chilima komanso akuluakulu ena asanu ndi atatu, mmagawo okwana atatu, ndipo kuti komiti yatsopanoyi ndiyomwe ipange kafukufuku wa gawo lomaliza pangoziyi.

“Mu pulani yanga yofufuza za ngoziyi, ndinakonza kuti pachitike kafukufuku oyang’anira mbali zitatu. Mbali yoyamba idali yofufuza kuti Kodi anatisiyawa chinawapha ndi chiyani, komanso kuwunikira ngati panali aliyense yemwe anali ndi moyo mundegemo itagwa.

Kafukufuku wachiwiri ali owunikira kuti Kodi chinagwetsa ndegeyi ndichani, ndipo mbali yachitatu ya kafukufuku wathu ndiyowunikira kuti Kodi zomwe zinachitika m’boma ndi zotani kuti ndege inagwayo ipite ulendo umenewu, komanso zinachitika m’boma ndi zotani kuti ndege idziwike kuti yasowa ndipo kuti iyang’anidwe mpaka kupezeka” anafotokozera motero Mtsogoleri wa dziko lino.

Koma Dr. Chakwera yemwe anati zamutengera masabata asanu ndi awiri kuti apeze mayina okhala mu komitiyi, walangiza komiti yatsopanoyi yomwe ikutsogozedwa ndi oweluza milandu, Justice Jabbar Alide, kuti igwire ntchito yake mosatengera mbali, mosatengeka ndi anthu a ndale ndi miseche, mosabisa kapena kuyikira wina kumbuyo, komanso masasungunula chilungamo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *