Akulu akale adati, _”Akulu ndi mdambo mozimira moto”._ Ndi angati mwa achinyamata alero amadziwa tanthauzo lenileni la mkuluwiko umenewu? Mmene a Vice President malemu Dr. Saulos Klaus Chilima (Mzimu Wawo Wuuse Mumtendere Wosatha) ankakonda kuyankhula miyambi zimasonyezeratu kuti Biyeni ankadziwa kufunika kosunga chikhalidwe cha makolo. Ankadziwa kuti anyamata ambiri sadziwa kulemekeza ndipo akuyenera kuphunzira khalidwe labwino la chi Malawi. A Chilima ankadziwa bwino lomwe kuti akuluakulu akale komanso omwe aliko lero amalangiza ana pamodzi ndi achinyamata kufunika kwake kosunga chikhalidwechi. Makolo athu adatiphunzitsa kuti tizikhala aulemu, kulemekeza makolo, kulemekeza aphunzitsi athu, kulemekeza agogo, kulemekeza mafumu, kulemekeza abusa komanso kulemekeza atsogoleri athu adziko komanso kulemekeza wina ndi mzake. Pamene demokalase idangoti balamanthu zikuoneka ngati kuti akuluakulu onse adatha ndipo adatsala ndi makanda osadziwa khalidwe labwino. Komatu demokalase pobwera idangofuna kutichotsera ife mchitidwe wankhanza pa ndale koma osati kuchotsa ulemu ndi chikhalidwe chathu ndi chamakolo ayi. Ndipo tanthauzo lenileni la demokalase ndiye kuti boma la anthu, olidyera ndi kulamulira ndi anthu omwewo. Osati izi zolamulidwa ndi atsamunda ayi. Demokalase sitanthauza kuchitira chipongwe anthu ena, kuononga katundu wa boma kapena wa anthu ena. Demokalase sitanthauza kutukwana anthu ena kapena kusalemekeza akulu. Ichi ndiye chifukwa chake a Chakwera ngakhale muwatukwane iwo sabwezera chipongwe ndipo satukwana munthu. Inu mudawamvapo a Dr. Bakili akutukwana? Nanga Masiteni Dr Joyce Banda mudawamvapo akutukwana? Mudawamverapo a Bingu akutukwana? Nanga izi zotukwana kapena kumakuwiza ndi kugenda atsogoleri adziko zachokera kuti? Kodi mumadziwa inu kuti mtsogoleri wa dziko lino ndiye tate komanso mfumu yadziko? Cholimbitsa mtima nchiyani kuti inu achinyamata mukhoza kutaya mwambo nkuyamba kutukwana tate wanu? Kodi mukhozadi inu kutukwana mayi wanu osalangidwa? Musayiwale kuti Mawu Woyera amati, _”Lemekeza atate wako ndi amako kuti achuluke masiku ako mdziko lomwe Mulungu adakupatsa.”_ Ngati demokalase simungayimvetsetse pitani ku ofesi ya kazembe wa Britain akakuphunzitseni momwe angerezi amalemekezera King Charles kapena Queen Elizabeth chifukwa ndiye makolo awo. Phunzirani khalidwe labwino. Siyani kunyoza ndikuchititsa manyazi mtsogoleri wa dziko lathu pamodzi ndi dziko lathu. Siyani kunyoza atsogoleri athu opuma monga Dr. Kamuzu Banda, Dr. Bakili Muluzi, Dr. Bingu wa Mutharika, Dr. Joyce Banda komanso Professor Arthur Peter Mutharika. Ichi sichikhalidwe chathu. Awa ndiye makolo athu pandale komanso mdziko. Tiyeni tizipereka ulemu ndi kusunga mwambo wamakolo ngakhale kuti titakhala anthu ochokera zipani zolamula kapena zotsutsa. Tilemekeze mtsogoleri wathu chifukwa ndiye tate wathu. Tikatero Mulungu adzatidalitsa komanso kutikweza. Kumbukirani Mau a Mulungu amati _”Chiyero chimakweza mtundu”._ Post navigation Is political violence part of DPP policy- MCP ask What next then , false accusers