A Namalomba kuyankhula kwa atolankhani Kusamvana kwabuka mchipani cha Democratic Progressive (DPP), pamene yemwe ali mkulu otsutsa kunyumba ya Malamulo a Kondwani Nankhumwa atemetsa nkhwangwa pa mwala kukana kuti iwo salola kusintha anthu omwe amayenera kukavota pa chisankho cha msonkhano waukulu omwe chipanichi chipangitse kumayambiriro a chaka cha 2024. A Nankhumwa awuza olemba nkhani kunyumba kwawo ku Luchenza ku Thyolo kuti ngati chipanichi chipitilire ndi ganizo limeneli iwo sachitila mwina koma kutengera nkhaniyi ku Bwalo la milandu. A Nankhumwa ati ali ndi umboni okwanila kuti pamsinkhano wa pa 13 December, 2023, ina mwa mfundo zomwe adagwiriana zinali zochotsa anthu pa mipando kuyambira ku constituency kufikila ku Regio n. A Nankhumwa ati kumeneku ndi kuphwanya malamulo omwe amayendetsa chipanichi. Nawo omwe amayankhula mchipanichi a Shadric Namalomba ati zomwe akunena Nankhumwa ndi zopanga pake ndipo iwo ati a Nankhumwa akungofuna kubweretsa chisokonezo mchipani. Post navigation A Malawi chuluka akupitilirabe kulandila chimanga chochuluka mdziko muno Malawi akupitilira kuchita bwino pankhani za ma ufulu osiyana siyana
This is DPP we know, fools , savages, full of hatred, non-democratic, why putting so many barriers? APM knows that he can lose against nankhumwa,as usual he wants to penetrate unlawful, and you praise him law professor? Total rubbish!! Nankhumwa is right and all of you trying to prevent nankhumwa are those people who made DPP fail. Namalomba is protecting his uncle,and he knows as APM win,he can be second chisale, I’ve never seen such pathetic party like DPP. Reply
Anankhumwa asowa chokamba akanafunsa vuto losafuna kugonja akaitanidwa ku nsonkhano wa akuluakulu achopani azipita azikanva okha osati azichita kuuzidwa Reply