Mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera lero wayamikila mpondamatiki wina otchuka yemwe amakhala m’mzinda wa Blantyre, kamba komanga chipatala chandalama zokwana K9Billion.

Polankhula m’mzinda wa Blantyre pamene iye amatsekulira chipatala chimenechi, Chakwera adapempha a Malawi wena kuti atengerepo chitsanzo chabwino chomwe a Mpinganjira awonetsa kumtumdu wa a Malawi.

A Chakwera ndi a Mpinganjira ku Blantyre

A Chakwera adauza mtundu wa a Malawi kuti ntchito yothana ndi matenda a Cancer imafunika kugwirana manja.

Iwo adati nkobvuta kuti boma palokha lingakwanitse kuthana ndi matenda amenewa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *