Chipani Cha Malawi Congress (MCP) chikupitilirabe kukhala chipani cha chikoka.

Tikunena pano pali mphekesera zochuluka zomwe zikusonyeza kuti mamulumuzana wena akuyembekezeka kulowa m’chipani cha Malawi Congress.

Wena omwe mphekesera zikusonyeza kuti alowa MCP ndi a Welani Chilenga, Ralph Mhone, Mganda Chiumia komanso katswiri odziwa kuyimba nyimbo zanthetemya zochemerera chipani a Miriam Chimbalanga nawo alowa MCP.

Malingana ndi malipoti omwe matsamba wena apa internet atsindikiza, anthuwa alandilidwa ndi chipani pompano.

Chipani cha MCP chakhala chikulandila anthu ambiri odziwika bwino pa ndale monga Wachiwiri kwa Mkulu wa nyumba ya malamulo a Mcheka Chilenje, Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) a Uladi Mussa , Wapampando wa chipani cha UTM mu chigawo cha pakati a Samson Mithenga ndi wena.

 

 

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *